Matthew 12:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku la chiweruzo anthu a ku Ninive adzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzaŵatsutsa. Paja iwowo adaatembenuka mtima, atamva malaliko a Yona. Ndipotu pano pali woposa Yona amene.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu a ku Ninive adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwake kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Ninive adzayimirira pachiweruzo ndi mʼbado uwu ndi kuwutsutsa pakuti iwo analapa Yona atalalikira ndipo tsopano wamkulu kuposa Yona ali pano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
1 Anthu a ku Nineve adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; cifukwa 2 iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwace kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Y ona ali pano.