Matthew 12:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku la chiweruzo mfumukazi yakumwera ija idzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno nidzaŵatsutsa. Paja iyo idaachita kuchokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva zolankhula zanzeru za mfumu Solomoni. Ndipotu pano pali woposa Solomoni amene.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo onani, wakuposa Solomoni ali pano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira pa tsiku lachiweruzo ndi mʼbado uwu ndipo idzawutsutsa pakuti inachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni, ndipo pano pali woposa Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
3 Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; cifukwa iye anacokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo; ndipo onani, wakuposa Solomo ali pano.