Matthew 12:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’ Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli zii, mosesasesa ndi mokonza bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo unena, Ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinatulukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo umati, ‘Ndidzabwerera ku nyumba yanga komwe ndinatuluka.’ Pamene ufika, upeza mopanda kanthu, mosesedwa ndi mokonzedwa bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo unena, ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinaturukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa.