Matthew 12:45 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iŵiri yoipa koposa uwowo, kenaka yonseyo imaloŵa nkukhazikika momwemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba. Zidzateronso ndi anthu ochimwa amakono.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka umapita kukatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa uwowo ndipo imapita ndi kukakhala mʼmenemo. Choncho khalidwe lotsiriza la munthu uyu limakhala loyipa kwambiri kuposa loyambalo. Umo ndi mmene zidzakhalire ndi mʼbado oyipawu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu yina inzace isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo 4 matsirizidwe ace a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ace. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.