Matthew 12:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ankalankhula ndi anthu ambirimbiri aja, nthaŵi yomweyo amai ake ndi abale ake adafika, naima panja. Ankafuna mpata woti alankhule naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yesu anali kuyankhulabe ndi gulu la anthu, amayi ndi abale ake anayimirira kunja, akufuna kuyankhulana naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Iye anali cilankhulire ndi makamu, onani, amace ndi 5 abale ace anaima panja, nafuna kulankhula naye.