Matthew 13:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu amene ali nkanthu kale, adzampatsanso zina, nadzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe kanthu, adzamlanda ngakhale kakang'onong'ono kamene ali nako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zowonjezera ndipo iye adzakhala nazo zambiri. Aliyense amene alibe, ngakhale zimene ali nazo adzamulanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zocuruka; koma yense amene alibe, cingakhale comwe ali naco cidzacotsedwa kwa iye.