Matthew 13:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi iwoŵa zikuchitikadi zimene mneneri Yesaya adaanena kuti, “ ‘Kumva mudzamva ndithu, koma osamvetsa, kuyang'ana mudzayang'ana ndithu, koma osapenya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzachitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati, Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa: “ ‘Kumva mudzamva koma osamvetsetsa. Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzacitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati. Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; Pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse;