Matthew 13:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu anthu ameneŵa nzeru zao nzobuntha, adagonthetsa makutu ao, ndipo adapsinya maso ao, kuwopa kuti angamapenye ndi maso aowo, angamamve ndi makutu aowo, angamamvetse ndi nzeru zaozo, ndi kutembenuka mtima, Ineyo nkuŵachiritsa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika, mʼmakutu mwawo ndi mogontha, ndipo atsinzina kuti asaone kanthu. Mwina angapenye ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka, Ineyo nʼkuwachiritsa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa unalemera mtima wa anthuawa, Ndipo m'makutu ao anamva mogontha, Ndipo maso ao anatsinzina; Kuti asaone konse ndi maso, Asamve ndi makutu, Asazindikire ndi mtima wao, Asatembenuke, Ndipo ndisawaciritse iwo.