Matthew 13:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu aliyense akamva mau onena za Ufumu wakumwamba, koma osaŵamvetsa, Woipa uja amabwera nkudzalanda zimene zidafesedwa mumtima mwake. Zimenezi ndiye mbeu zogwera m'njira zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene aliyense akumva uthenga wa ufumu koma sawuzindikira, woyipayo amabwera ndi kuchotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Iyi ndi mbewu yofesedwa mʼmbali mwa njira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu ali yense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula cofesedwaco mumtima mwace. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.