Matthew 13:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangolimbika kanthaŵi pang'ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthaŵi yomweyo munthuyo amabwerera m'mbuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma popeza alibe muzu, iwo amakhala nthawi yochepa. Pamene vuto kapena zunzo libwera chifukwa cha mawu, iye amagwa mofulumira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo cifukwa ca mau, iye akhumudwa pomwepo.