Matthew 13:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene mmera udakula nkuyamba kuchita njere, namsongole uja nayenso adayamba kuwoneka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene tirigu anamera ndi kutulutsa ngala, namsongole anaonekanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene mmera unakula, nubala cipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole.