Matthew 13:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m'munda mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuza fanizo lina kuti, “Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pace;