Matthew 13:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuzanso fanizo lina nati: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza mu ufa wambiri mpaka wonse unafufuma.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi cotupitsa mikate, cimene mkazi anacitenga, nacibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.