Matthew 13:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yesu adaŵasiya anthu ambirimbiri aja, nakaloŵa m'nyumba. Tsono ophunzira ake adadzampempha kuti, “Tatimasulirani fanizo la namsongole wam'munda lija.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Iye anasiya gulu la anthu ndi kukalowa mʼnyumba. Ophunzira ake anapita kwa Iye nati, “Timasulireni fanizo la namsongole mʼmunda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ace anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.