Matthew 13:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m'munda. Munthu wina atachitumba, amachibisanso. Kenaka mokondwa amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula munda uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi cuma cobisika m'munda; cimene munthu anacipeza, nacibisa; ndipo m'kucikonda kwace acoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.