Matthew 13:52 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Iye adaŵauza kuti, “Nchifukwa chaketu mphunzitsi aliyense wa Malamulo, amene adaphunzira za Ufumu wakumwamba, ali ngati mwinibanja amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zinthu zakale m'nkhokwe ya chuma chake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake, mlembi aliyense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m'chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuza kuti, “Chifukwa chake mphunzitsi aliyense wa malamulo amene walangizidwa za ufumu wakumwamba ali ngati mwini nyumba amene amatulutsa chuma chatsopano komanso chakale.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye anati kwa iwo, Cifukwa cace, mlembi ali yense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene aturutsa m'cuma cace zinthu zakale ndi zatsopano.