Matthew 13:54 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika ku dera lakwao, adayamba kuphunzitsa anthu m'nyumba yao yamapemphero. Amene ankamumva ankadabwa nkumati, “Kodi Iyeyu, nzeru zimenezi ndi mphamvuzi adazitenga kuti?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika kudziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika ku mudzi kwawo anayamba kuphunzitsa mʼmasunagoge awo ndipo iwo anadabwa nati, “Munthu uyu anayitenga kuti nzeru iyi ndi mphamvu zodabwitsazi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 3 pofika ku dziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitengakuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi?