Matthew 14:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yamadzulo ophunzira ake adadzamuuza kuti, “Kunotu nkuthengo, ndipo ano ndi madzulo. Auzeni anthuŵa azinyamuka, apite ku midzi kuti azikagula chakudya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ake anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ace anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga cipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite ku midzi kukadzigulira okha kamba.