Matthew 14:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatero, adalamula kuti anthu aja akhale pansi pa udzu. Tsono adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake, ophunzira aja nkukagaŵira anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi pamaudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.