Matthew 14:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Madzulo omwewo Yesu adalamula ophunzira ake kuti aloŵe m'chombo, atsogole kupita ku tsidya, pamene Iye akuuza anthu kuti azipita kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye kutsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye ku tsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.