Matthew 14:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende cifukwa ca Herodiya, mkazi wa mbale wace Filipo.