Matthew 14:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu akumeneko adamzindikira Yesu, nakadziŵitsa anzao a ku dera lonse lozungulira pamenepo. Motero adadza kwa Yesu ndi anthu onse odwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene amuna a pamenepo anamzindikira, anatumiza konse kudziko lonse lozungulira, nadza nao kwa Iye onse akukhala ndi nthenda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'meneamuna a pamenepo anamzindikira, anatumiza konse ku dziko lonse lozungulira, nadzanao kwa Iye onse akukhala ndi nthenda;