Matthew 15:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mai wina wachikanani, wa ku madera amenewo, adadza kwa Yesu. Adafuula kuti, “Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi ngwogwidwa koopsa ndi mzimu woipa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anaturuka m'malire, napfuula, nati, Mundicitire ine cifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi ciwanda.