Matthew 15:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu sadamuyankhe mau ndi amodzi omwe. Ophunzira ake adadza nampempha kuti, “Muuzeni azipita, onani akubwera natisokosera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Iye sanamyankhe mau amodzi. Ndipo ophunzira ake anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, “Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Iye sanamyankha mau amodzi. Ndipo ophunzira ace anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti apfuula pambuyo pathu.