Matthew 15:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu onse adadabwa poona kuti osalankhula aja akulankhula, olumala aja achira, opunduka miyendo aja akuyenda, ndipo akhungu aja akupenya. Choncho adatamanda Mulungu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ataona osayankhula akuyankhula, ofa ziwalo akuchira, olumala miyendo akuyenda ndi osaona akuona anadabwa kwambiri. Ndipo analemekeza Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nacira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.