Matthew 16:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga bwanji simukuzindikira kuti sindimanena za buledi? Chenjera nachoni chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi Asaduki.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Bwanji nanga simudziwa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma pewani chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitheka bwanji kuti inu simukumvetsetsa kuti Ine sindinkayankhula nanu za buledi? Koma inu chenjerani ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Bwanji nanga simudziwa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma pewani cotupitsa ca Afarisi ndi Asaduki.