Matthew 16:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga pa dziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula pa dziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo cimene ukamanga pa dziko lapansi cidzakhala comangidwa Kumwamba: ndipo cimene ukacimasula pa dziko lapansi, cidzakhala comasulidwa Kumwamba.