Matthew 16:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Pamene dzuŵa likuloŵa, mumati, ‘Maŵa kucha bwino, popeza kuti kumwamba kuli psuu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Madzulo munena, Kudzakhala ngwee; popeza thambo lili lacheza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Kunja kukamada, inu mumati, kudzakhala nyengo yabwino popeza thambo ndi lofiira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Madzulo munena, Kudzakhala ngwe; popeza thambo liri laceza.