Matthew 16:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wace? kapena munthu adzaperekanji cosintha ndi moyo wace?