Matthew 16:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo m'maŵa mumati, ‘Lero ndiye kugwa mvula yamkuntho, popeza kuti kumwambaku kwachita mitambo yabii.’ Mumatha kutanthauzira m'mene kukuwonekera kumwambaku, koma osatha kutanthauzira zizindikiro za nthaŵi zino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo yino, simungathe kuzindikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mmawa mumati, ‘Lero kudzakhala mvula yamphepo popeza thambo ndi lofiira ndi mitambo ya mvula.’ Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a thambo koma simungathe kutanthauzira zizindikiro za nthawi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo; popeza thambo liri la ceza codera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo yin o, simungathe kuzindikira.