Matthew 16:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a mbadwo woipa ndi wosakhulupirika amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzaona chizindikiro china kupatula chokha chija cha mneneri Yona.” Atatero, Yesu adaŵasiya nachokapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya, nachokapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼbado woyipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro chodabwitsa koma palibe ngakhale chimodzi chidzapatsidwa kupatula chizindikiro cha Yona.” Pamenepo Yesu anawasiya nachoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Obadwa oipa ndi acigololo afunafuna cizindikiro; ndipo sadzalandira cizindikiro cina, koma cizindikiro ca Yona. Ndipo Iye anawasiya, nacokapo.