Matthew 16:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi mpaka pano simunamvetsebe? Kodi simukukumbukira kuti ndi buledi msanu ndidadyetsa anthu zikwi zisanu? Nanga mudaadzaza madengu angati ndi zotsala?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi chikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi madengu angati munawatola?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kodi cikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi mitanga ingati munaitola?