Matthew 17:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adati, “Ambuye mchitireni chifundo mwana wanga. Ali ndi khunyu ndipo amavutika koopsa. Kaŵirikaŵiri amagwa pa moto mwinanso m'madzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala nkhunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye, citirani mwana wanga cifundo; cifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawiri kawiri pamoto, ndi kawiri kawiri m'madzi.