Matthew 17:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Kapernao, okhometsa msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu adadzafunsa Petro kuti, “Kodi aphunzitsi anuŵa sakhoma msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika ku Kapernao amene aja akulandira ndalama za ku Kachisi anadza kwa Petro nati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofika ku Kapernao arnene aja akulandira ndalama za kukacisi anadza kwa Petro nati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo?