Matthew 17:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kuwopa kuŵakhumudwitsa a ku Nyumba ya Mulunguŵa, kaŵedze nsomba ku nyanja. Nsomba imene ukayambire kuŵedza, ukaikanule kukamwa, ndipo ukapezamo ndalama. Ukatenge ndalamayo nkukakhomera msonkho wanga ndi wako womwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamtu pa iwe ndi Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pace udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamtu pa iwe ndi Ine.