Matthew 17:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akulankhula choncho, kudadza mtambo woŵala nuŵaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akali cilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphi mba iwo: ndipo onani, mau alikunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.