Matthew 18:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya cipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba. [