Matthew 18:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono mukuganiza bwanji? Munthu atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nkutayika, kodi sangasiye 99 zina zija m'phiri nkukafunafuna imodzi yotayikayo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanga muyesa bwanji? Ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi nʼkusowa, kodi sasiya 99 zija mʼmapiri ndi kupita kukafuna imodzi yosocherayo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanga muyesa bwanji? ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu manu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo?