Matthew 18:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye popeza kuti adaasoŵa chobwezera ngongoleyo, mbuye wake uja adalamula kuti amgulitse wantchitoyo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake ndi zake zonse, kuti ngongole ija ibwezedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza sakanatha kubweza, bwanayo analamula kuti iye, mkazi wake, ana ake ndi zonse anali nazo zigulitsidwe kuti zibweze ngongoleyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wace analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wace ndi ana ace omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.