Matthew 18:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma pamene wantchitoyo ankatuluka, adakumana ndi mmodzi mwa antchito anzake, yemwe iye adaamkongoza ndalama zochepa. Adamgwira pa khosi mwaukali namuuza kuti, ‘Bweza ngongole yako ija.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma wantchito uja atatuluka, anakumana ndi wantchito mnzake amene anakongola kwa iye madinari 100. Anamugwira, nayamba kumukanyanga pa khosi, namuwumiriza nati, ‘Bwezere zimene unakongola kwa ine!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kapolo uyu, poturuka anapeza wina wa akapolo anzace yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera cija unacikongola.