Matthew 18:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Antchito anzake ena ataona zimenezi, adamva chisoni kwambiri. Adapita kukafotokozera mbuye wao zonsezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake m'mene akapolo anzake anaona zochitidwazo, anagwidwa chisoni chachikulu, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinachitidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene antchito ena anaona zomwe zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita nakawuza bwana wawo zonse zimene zinachitika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace m'mene akapolo anzace anaona zocitidwazo, anagwidwa cisoni cacikuru, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinacitidwa.