Matthew 19:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena ankabwera ndi ana kuti Yesu aŵasanjike manja ndi kuŵapempherera, ophunzira ake nkumaŵazazira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo anabwera nawo ana kwa Yesu kuti awasanjike manja ndi kuwapempherera. Koma ophunzira ake anadzudzula amene anabweretsa anawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ace pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.