Matthew 19:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene munthu uja adamva mau ameneŵa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa anali wolemera kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mnyamatayo m'mene anamva conenaco, anamuka wacisoni; pakuti anali naco cuma cambiri.