Matthew 2:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaloŵa m'nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake, ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira Iye. Pomwepo anamasula chuma chawo ndi kupereka mphatso zawo za ndalama zagolide, lubani ndi mure.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofika ku nyumba anaona kamwanako ndi Mariya amace, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula cuma cao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure.