Matthew 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atapita akatswiri a nyenyezi aja, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto. Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, uthaŵire ku Ejipito. Ukakhale kumeneko mpaka ndidzakuuze, popeza kuti Herode azidzafunafuna mwanayu kuti amuphe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atachoka, taonani mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto nati, “Tadzuka, tenga mwanayo pamodzi ndi amayi ake ndipo muthawire ku Igupto. Mukakhale kumeneko mpaka nditakuwuza pakuti Herode adzafunafuna mwanayo kuti amuphe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene iwo anacoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amace, nuthawire ku Aigupto, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.