Matthew 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira, kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Ndidaitana Mwana wanga kuti atuluke ku Ejipito.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke m'Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira. Ndipo zinakwaniritsidwa zomwe ananena Ambuye mwa mneneri kuti, “Ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti cikacitidwe conenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga aturuke m'Aigupto.