Matthew 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Herode atazindikira kuti akatswiri a nyenyezi aja adampusitsa, adatuma anthu ku Betelehemu ndi ku midzi yonse yozungulira, kuti akaphe ana aamuna onse a zaka ziŵiri kapena kucheperapo. Zaka zimenezi adaaŵerengera potsata m'mene adaamvera kwa akatswiri aja za nthaŵi imene iwowo adaaiwonera nyenyeziyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta m'Betelehemu ndi ta m'milaga yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Herode atazindikira kuti Anzeruwo anamupusitsa, anakwiya kwambiri. Ndipo anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna a mʼBetelehemu ndi midzi yozungulira amene anali a zaka ziwiri kapena zocheperapo, molingana ndi nthawi imene Anzeruwo anamuwuza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta m'Betelehemu ndi ta m'miraga yace yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.