Matthew 2:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma atamva kuti Arkelao ndiye mfumu ya ku Yudeya m'malo mwa bambo wake Herode, adaopa kupita kumeneko. Tsono atalandira chenjezo kwa Mulungu m'maloto, adapita ku dera la Galileya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pakumva iye kuti Arkelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wake Herode, anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anachenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa kudziko la Galileya,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma atamva kuti Arikelao akulamulira mu Yudeya mʼmalo mwa abambo ake, Herode, anaopa kupitako. Atachenjezedwa mʼmaloto, anapita ku Galileya,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pakumva iye kuti Arikelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wace Herode, anacita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anacenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa ku dziko la Galileya,