Matthew 2:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Herodeyo adasonkhanitsa akulu onse a ansembe ndi aphunzitsi onse a Malamulo a Mose, naŵafunsa kuti, “Kodi paja adati Mpulumutsi wolonjezedwa ndi Mulungu uja adzabadwira kuti?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe aakulu onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Khristuyo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anayitanitsa anthu onse, akulu ansembe ndi aphunzitsi amalamulo nawafunsa kuti, “Kodi Khristu adzabadwira kuti?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe akuru onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Kristuyo?