Matthew 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“ ‘Iwe Betelehemu wa m'dziko la Yuda, sindiwe wamng'ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda. Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri pamene adzalamulira anthu anga Aisraele.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma iwe Betelehemu, chigawo cha Yudeya, sindiwe wamngʼonongʼono mwa olamulira a Yudeya; pakuti otsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraeli.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe: Betelehemu, dziko la Yudeya, Sukhala konse wamng'onong'ono mwa akuru a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzacokera mwaiwe, Amene adzaweta anthu anga Aisrayeli.